Zaife

Site Map

Mbiri yathu

Hotel, Food Processing and Catering Workers Union (HFPCWU) kapena kuti Hotels Union ndi bungwe la mgwirizano wa ogwira ntchito, pachingelezi amati trade union lomwe Iimawo- na za ufulu wa anthu ogwira ncthito mumahotela, malo okonza zakudya ndi zakumwa zosi- yana siyana, malo odyera, ndiponso ogona. Bungweli lidayamba chaka cha 1993.

Mu chaka cha 1995 bungweli linalembetsedwa (register) kuboma kudzera ku unduna woona za anthu ogwira ntchito la Ministry of Labour and Vocational Training (MOLVT). Chaka chomwecho masankho anachitidwa ku mount soche Hotel mu chipinda cha Njamba mu mzinda wa Blantrye. Ndipo yuniyoni imeneyi inali yoyamba kusankha mayi kukhala pa udindo wa mlembi wamkulu pambiri ya mayuniyoni m’MaIawi. Bungweli linalinso loyamba kukumbukira tsiku la anthu apantchito pa 1 May 1994. Bungweli linatenganso mbali kuyam- bitsa bungwe la Malawi Congress of Trade Unions (MCTU) kulowa malo mwa Trade Union Congress of Malawi (TUCM) lomwe lili bungwe IaIikuIu lowona za ufulu wa anthu ogwira ntchito muno m’MaIawi. Izi ndi zina zomwe bungweli lachita.

 

Zolinga zathu

Zina mwa zolinga za yuniyoni imeneyi ndi izi:

  1. Kuteteza ufulu wa anthu ogwira ntchito
  2. Kusamalira myoyo ya anthu ogwira ntchito
  3. Kukometsa malamulo ogwilira ntchito
  4. Kuwonetsa kuti padzikhala mtendere ndi ngwirizano pa malo ogwilira ntchito: pakati pa mabwana ndi ogwira ntchito ndiponso pakati pa ogwira ntchito okhaokha
  5. Kukweza dziko

Kodi Malamulo akutinji za mgwirizano ya ogwira ntchito?

Malamulo a dziko lino akulola kuyambitsa mabungwe a Trade Union zimene zili mu buku IaIikuIu Ia malamulo a dziko lino lotchedwa konsitishoni (constitution of Malawi). Zili pa ndime 31(2) ya konsitishoni ndiponso M’MalamuIo a ntchito lotchedwa (Labour Act) la 1996
ndime 4.

Anthu ogwira ntchito asaope, umunthu aliyense kaya olemba ntchito (mabwana) chifukwa umenewu ndi ufulu wa munthu wapantchito umene ndiwotetezedwa ndi malamulo adziko lino.

Kodi HFPCWU (Hotels Union) Membala wa bungwe lina?

Hotel Union ndi bungwe loyima palokha koma limangwira ntchito ndi mabungwe ena omwe ali ndi zolinga zofanana nalo. Yuniyoni ndi membela wa Malawi Congress of Trade Unions (MCTU). Dziko la Malawi lili ndi mabungwe akuluakulu awiri (ma federation) omwe amagwira ntchito ndi mayuniyoni ang’onoang’ono (National Unions). Awa ndi Malawi Congress of Trade Unions (MCTU) ndi National Federation of Trade Unions (NAFETU).
MCTU iii ndi mammbembala a muyuniyoni ang’ono ang’ono okwana 26 kuphatikizapo Hotel Union, pamene NAFETU ili ndi mamembala ocheperapo. Hotel Union ili pa ubale ndi mabungwe a kunja kwa dziko lino awa:

  • IUF: International Union of Food yomwe likulu lake lili ku Geneva ku Switzerland ndipo lili ndi nthambi yake ku Africa yomwe amaofesi ake ali muzinda wa Cape Town ku South Africa
  • FGTB: Belgian General Federation of Labour la ku Belgium
  • HORVAL: Food, Hotel and Catering Workers of Belgium
  • ISVI: International Syndicaal
  • 3F United Federation of Danish
  • Trade Union Solidarity Centre of Finland (SASK)

Kodi membala wa union ndi yani?

Membala wa yuniyoni ndi munthu amene walowa bungwe limeneli polemba chikalata (fomu) ndipo amapeleka ndalama za umembala mwezi ndi mwezi. Ndalama ya pamweziyi ndi 1% ya malip- iro a mwezi umodzi a membala aliyense. Mem- balayu atha kupereka ndalama zake kudzera podulidwa malipiro kukampani (check of system) ndipo akakumpani amalemba cheke chimodzi chandalama zomwe zadulidwa kwa mamembala ndikutumiza ku yuniyoni.

Kodi ma membala ena a Hotels Union ali kuti?

Hotel union ndi ya anthu a panchito amene amangwira makapani wopanga zakudya, za- kumwa, malo ogona ndi kumwera ngakhaleso mabekale, makalabu, mamotelo, magesiti- hausi, maloji, maresitolanti, ndi ena  Ndipo makapani amenewa ngati antchito ake ali pamavuto, a Hotel Union amafungatira kuti zonse zidziyenda bwino. Yuniyoni ikupanga zazi- kulu pochititsa kuti anthu ena abwerezeredwe patchito atachotsedwa, anthu enanso kulipidwa malipiro awo patapita nthawi yaitali atachosedwa ntchito. Yuniyoni simafuna kumva kuti anthu amene ali mamembala ake akuzunzidwa kapena kuzunzika kuntchito.

 

Mau kuchokera kwa mlembi wankulu

Maphunziro a ufulu wa anthu apantchito akufinika kuno Malawi, izi zili chonchi chifukwa choti boma la ulamuliro wachipani chimodzi linkaponderaza ogwira ntchito. Poti tsopano kuli ulamuliro wa zipani zambiri, nkofunika kuphunzitsa ogwira ntchito kuti atsekule maso kuti atenge nawo mbali pachitukuko cha fuko la Malawi. M'malo mwa atsogoleri anzanga a bungwe la Hotel, Food Processing and Catering Workers Union (HFP- CWU) ndiyamike bungwe la Trade Union Solidarity Centre (SASK) aku Finland, potipatsa chithandizo cha ndalama. Zikomo nonse.

“Ntchito ndi mumtengo, itha kutha nthawi ina iliyonse! Kodi munayamba mwamvapo kapena kuwona wina atauzidwa kuti ntchito yatha popanda chidziwitso kapena chifukwa chenicheni; mwinanso osaudzidwa chifukwa chomwe ntchi- toyo yathera? Zoterezi zitakuchitikirani mungatani? Dziwani kuti zimenezi zitha kuchitikira aliyense. Dziwani za ufulu wanu! Pezani nkhoswe yanu lero!”

Union ndi Nkhoswe

Pantchito pakakhala mavuto, mavutowa ayenera kuperekedwa ku yuniyoni kudzera kwa at- sogoleri a bulanchi (pamalo ogwira ntchito). Atsogoleri amatenga mavutowo kapena madandaulowo kupita nawo kwa mabwana kuti akambirane ndikupeza njira yothetsera mavutowo limodzi. Ngati madandaulowo sangakonzedwe pa bulanchi, atsogoleri amakatula madandaulowo ku ofesi ya yuniyoni. Akuofesi akalephera nkhani nawonso amaitumiza ku boma kudzera kwa mlembi wamkulu wa nduna wa Ministry of Labour and Vocational Train- ing (MOLVT). Ngati pakhalabe kusagwirizana pakati pa mabwana ndi a yuniyoni, a yuniyoni amaitenga nkhaniyo kukhoti la anthu ogwira ntchito ndi olemba ntchito la Industrial Rela- tions Court (IRC), kukhotiko ndikumene amapereka chigamulo poyang’anira malamulo a pantchito.